adplus-dvertising
Malawi

Apolisi awaphunzitsa momwe angachepetsere nkhanza zokhudza kugonana

Wachiwiri kwa mkulu woona chitetedzo cha m’madera akumidzi kunthambi ya a Police m’dziko muno Senior Supritendent Albert Nyongani wapempha a Police kuti adziyendera kawirikawiri malo (misasa) omwe anthu okhudzidwa ndi ngozi zokugwa mwadzidzidzi amakhala pofuna kuthana ndi nkhanza zokhudza kugonana komanso nkhanza zina zomwe anthuwa amakumana nazo.

Supritendent Nyongani amayankhula izi ku Police ya Machinga komwe amakambirana ndi apolisi momwe angatetedzere nkhanza zokhudza kugonana komanso nkhanza zina zomwe zimachitika m’madera omwe mumachitika ngozi zokugwa mwadzidzidzi.

Iwo ati kuyendera kawiri kawiri mmalo omwe anthu okhudzidwa ndi ngozi zokugwa mwadzidzidzi komanso kuyendera madera akumidzi kumapangitsa kuti nkhanza zizichepa chifukwa anthu omwe amaganidza kuchita za upandu amachita mantha akawona a Police akuyendayenda mdelaro.

Pamenepa Supritendent Nyongani adati poyendera madera angoziwo ayenera kumayendera limodzi ndi komiti yowona zachitetezo chamadera akumudzi (community policing) popeza ndiwomwe amapereka chitetezo chakumudzi.

“Kuyendera madera akumudzi (patrol) kumapangitsa kuti umbanda ndi umbava komanso mchitidwe wokhudza nkhanza zogonana madera momwe mumachitika ngozi zokugwa mwadzidzidzi uchepe,” datero Senior Supritendent Nyongani.

Mu mau ake Inspector Naison Chibondo yemwe ndiwa Police woona chitetedzo cham’madera akumudzi Boma la Zomba komanso ndiyemwe adali mmodzi wophunzitsa patsikulo adati mchitidwe wokhudza nkhanza zogonana m’madera momwe mumachitika ngozi zokugwa mwadzidzidzi ukumachulukira chifukwa mmalo omwe mumagona anthu okhudzidwawo apolisi samayenderamo.

Iye adalimbikitsa apolisi omwe adalandira maphunziriwo kuti akadzigwiritse ntchito zomwe aphunzirazo akapita kumadera kwao komwe amagwilira ntchito.

Follow us on Twitter:

WATCH NOW

DOWNLOAD NOW